1 Akulu tsono mwa inu ndiwadandaulira, ine mkulu mnzanu ndi mboni ya zowawa za Kristu, ndinenso wolawana nao ulemerero udzabvumbulutsikawo:
2 Wetani gulu la Mulungu liri mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokangamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwacangu;
3 osati monga ocita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.
4 Ndipo pakuonekera Mbusa wamkulu, mudzalandira korona wa ulemerero, wosafota. Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu.
5 Koma nonsenu mubvale kudzicepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa cisomo kwa odzicepetsa.
6 Potero dzicepetseni pansi pa dzanja la mphamvu lao Mulungu, kuti panthawi yace akakukwezeni;
7 ndi kutaya pa iye nkhawa yanu yonse, pakuti iye asamalira inu.
8 Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
9 ameneyo mumkanize okhazikika m'cikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zirimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.
10 Ndipo Mulungu wa cisomo conse, amene adakuitanani kulowa ulemerero wace wosatha mwa Kristu, mutamva zowawa kanthawi, adzafikitsa inu opanda cirema mwini wace, adzakhazikitsa, adzalimbikitsa inu.
11 Kwa iye kukhale mphamvu ku nthawi za nthawi. Amen.
12 Mwa Silvano, mbale wathu wokhulupirika monga ndimayesa, ndalembera kwa inu mwacidule, ndi kudandaulira, ndi kucita umboni, kuti cisomo coona ca Mulungu ndi ici; m'cimeneci muimemo.
13 Iye wa ku Babulo wosankhidwa pamodzi nanu akulankhulani; ateronso Marko mwana wanga.
14 Lankhulanani ndi cipsompsono ca cikondi.Mtendere ukhale ndi inu nonse muli mwa Kristu.