1 Petro 2 BL92

1 Momwemo pakutaya coipa conse, ndi cmyengo conse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kadoka, ndi masiniiriro onse,

2 lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda cinyengo, kuti mukakule nao kufikira cipulumutso;

3 ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima;

4 amene pakudza kwa iye, mwala wamoyo, wokanidwatu ndi anthu, koma ndi Mulungu wosankhika, waulemu,

5 inunso ngati miyala yamoyo mumangidwa nyumba ya uzimu, kun mukhale ansembe oyera mtima, akupereka nsembe zauzimu, zolandiridwa ndi Mulungu mwa Yesu Kristu,

6 Cifukwa kwalembedwa m'lembo,Taona, ndiika m'Ziyoni mwala wotsiriza wa pangondya, wosankhika, wa mtengo wace;Ndipo wokhulupirira iye sadzanyazitsidwa.

7 Kwa inu tsono akukhulupira, ali wa mtengo wace; koma kwa iwo osakhulupira,Mwala umene omangawo anaukana,Womwewo unayesedwa mutu wa pangondya;

8 ndipo,Mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lopunthwitsa;kwa iwo akukhumudwa ndi mau, pokhala osamvera, kumenekonso adaikidwako.

9 Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mw ni wace, kotero kuti mukalakire zoposazo za iye amene anakuitanani muturuke mumdima, mulowe kuunika kwace kodabwitsa;

10 inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandira cifundo, koma tsopano mwalandira cifundo.

Za mayendedwe ao pakati pa akunja, Asonle kwa akuru

11 Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zicita nkhondo pa moyo;

12 ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ocita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona nchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.

13 Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, cifukwa ca Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse;

14 kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ocira zoipa, koma kusimba ocita zabwino.

15 Pakuti cifuniro ca Mulungu citere, kuti ndi kucita zabwino mukatontholetse cipulukiro ca anthu opusa;

16 monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga cobisira coipa, koma ngati akapolo a Mulungu.

17 Citirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Citirani mfumu ulemu.

Zoyenera anyamata Akristu

18 Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali.

19 Pakuti ici ndi cisomo ngati munthu, cifukwa ca cikumbu mtima pa Mulungu alola zacisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.

20 Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pocimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pocita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko cisomo pa Mulungu.

21 Pakuti kudzacita ici mwaitanidwa; 1 pakutinso Kristu anamva zowawa m'malo mwanu, 2 nakusiyirani citsanzo kuti mnkalondole mapazi ace;

22 3 amene sanacita cimo, ndipo m'kamwa mwace sicinapezedwa cinyengo;

23 4 amene pocitidwa cipongwe sanabwezera cipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma 5 anapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama;

24 6 amene anasenza macimo athu mwini yekha m'thupi mwace pamtanda, kuti ife, 7 titafa kumacimo, tikakhale ndi moyo kutsata cilungamo; 8 ameneyo mikwingwirima yace munaciritsidwa nayo.

25 Pakuti 9 munalikusocera ngati nkhosa; koma rsopano mwabwera kwa 10 Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu.

Mitu

1 2 3 4 5