1 Petro 3 BL92

Zoyenera akazi ndi amuna

1 Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu ainu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi;

2 pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.

3 Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala cobvala;

4 koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.

5 Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha;

6 monga Sara anamvera Abrahamu, namucha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ace ngati mucita bwino, osaopa coopsa ciri conse.

7 Momwemonso amuna inu, khalani nao monga mwa cidziwitso, ndi kucitira mkazi ulemu, monga cotengera cocepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa cisomo ca moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.

Za cikondano, Za kulola masautso monga anacita Ambuye

8 Cotsalira, khalani nonse a mdma umodzi, ocitirana cifundo, okondana ndi abale, acisoni, odzicepetsa:

9 osabwezera coipa ndi coipa, kapena cipongwe ndi cipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ici mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.

10 Pakuti,iye wofuna kukonda moyo,Ndi kuona masiku abwino,Aletse lilime lace lisanene coipa,Ndi milomo yace isalankhule cinyengo;

11 j Ndipo apatuke pacoipa, nacite cabwino;Afunefune mtendere ndi kuulondola.

12 Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama,Ndi makutu ace akumva rembedzo lao;Koma nkhope ya Ambuye iri pa ocita zoipa,

13 Ndipo ndani iye amene adzakucitirani coipa, ngati mucita naco cangu cinthu cabwino?

14 Komatu ngatinso mukamva zowawa cifukwa ca cilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa;

15 koma mumpatulikitse Ambuye Kristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kucita codzikanira pa yense wakukufunsani cifukwa ca ciyembekezo ciri mwa inu, komatu ndi cifatsondi mantha;

16 ndi kukhala naco cikumbu mtima cabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Kristu akacitidwe manyazi.

17 Pakuti, kumva zowawa cifukwa ca kucita zabwino, ndi kumva zowawa cifukwa ca kucita zoipa, nkwabwino kumva zowawa cifukwa ca kucita zabwino, ngati citero cifuniro ca Mulungu,

18 Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma woparsidwa moyo mumzimu;

19 m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende,

20 imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka cingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;

21 cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu;

22 amene akhala pa dzanja lamanja la Mulungu, atalowa m'Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zomgonjera.

Mitu

1 2 3 4 5