1 Petro 1 BL92

1 PETRO, mtumwi wa Yesu Kristu, kwa osankhidwa akukhala: alendo a cibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya,

2 monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m'ciyeretso ca Mzimu, cocitira cimvero, ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu: Cisomo, ndi mtendere zicurukire inu.

Ciyamiko cifukwa ca cipulumutso

3 Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye amene, monga mwa cifundo cace cacikuru, anatibalanso ku ciyembekezo ca moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu;

4 kuti tilandire colowa cosabvunda ndi cosadetsa ndi cosafota, cosungikira m'Mwamba inu,

5 amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa cikhulupiriro, kufikira cipulumutso cokonzeka kukabvumbulutsidwa nthawi yotsiriza.

6 M'menemo mukondwera, kungakhale tsopano kanthawi, ngati kuyenera, mukacitidwe cisoni ndi mayesero a mitundu mitundu,

7 kuti mayesedwe a cikhulupiriro canu, ndiwo a mtengo wace woposa wa golidi amene angotayika, ngakhale ayesedwa ndi moto, akapezedwe ocitira ciyamiko ndi ulemerero ndi ulemu pa bvumbulutso la Yesu, Kristu;

8 amene mungakhale simunamuona mumkonda; amene mungakhale simumpenya tsopano, pokhulupirira, mukondwera naye ndi, cimwemwe cosaneneka, ndi ca ulemerero:

9 ndi kulandira citsiriziro ca cikhulupiriro canu, ndico cipulumutso ca moyo wanu.

10 Kunena za cipulumutso ici anafunafuna nasanthula aneneri, pakunenera za cisomo cikudzerani;

11 ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Kristu wokhala mwa iwo analozera, pakucitiratu umboni wa masautso a Kristu, ndi ulemerero, worsarana nao.

12 Kwa iwo amene kudabvumbulutsidwa, kuti sanadzitumikira iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kucokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.

Awadandaulira atsate kuyeramtima

13 Mwa ici, podzimanga m'cuuno, kunena za mtima wanu, mukhale odzisunga, nimuyembekeze konse konse cisomo cirikutengedwa kudza naco kwa inu m'bvumbulutso la Yesu Kristu;

14 monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu;

15 komatu monga iye wakuitana inu ali woyera mtima, khaiani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse;

16 popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

17 Ndipo mukamuitana ngati Alate, iye amene aweruza monga mwa nchito ya yense, wopanda tsankhu, khalani ndi mantha nthawi ya cilendo canu;

18 podziwa kuti simunaomboledwa ndi zobvunda, golidi ndi siliva, kusiyana nao makhalidwe anu acabe ocokera kwa makolo anu:

19 koma 1 ndi mwazi wa mtengo wace wapatali 2 monga wa mwana wa nkhosa wopanda cirema, ndi wopanda banga, ndiwo mwazi wa Kristu:

20 3 amene anazindikirikatu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa citsiriziro ca nthawi,

21 cifukwa ca inu amene mwa rye mukhulupirira Mulungu 4 wakwnuukitsa iye kwa akufa, ndi kumpatsa iye ulemerero; kotero kuti cikhulupiriro canu ndi ciyembekezo canu cikhale pa Mulungu.

22 Popeza 5 mwayeretsa moyo wanu pakumvera coonadi kuti 6 mukakonde abale ndi cikondi cosanyenga, mukondane kweni kweni kucokera kumtima;

23 7 inu amene mudabadwanso, osati ndi mbeu yofeka, komatu yosaola, mwa mau a Mulungu amoyo ndi okhalitsa.

24 Popeza,8 Anthu onse akunga udzu,Ndi ulemerero waowonse ngad duwa la udzu.Udzuwo ungotota, ndi duwa lace lingogwa;

25 9 Koma Mau a Mulungu akhala cikhalire.Ndipo 10 mau olalikidwa kwa Inu ndi jawo.

Mitu

1 2 3 4 5