Yakobo 5 BL92

Acuma ouma mtima atsutsidwa

1 Nanga tsono acuma inu, lirani ndi kucema cifukwa ca masautso anu akudza pa inu,

2 Cuma canu caola ndi zobvala zanu zajiwa ndi njenjete.

3 Golidi wanu ndi siliva wanu zacita dzimbiri, ndipo dzimbiri lace lidzacita mboni zoneneza Inu ndipo zidzadya nyama yanu ngat: moto. Mwadzikundikira cuma masiku otsiriza.

4 Taonani, mphotho ya anchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ipfuula; ndipo mapfuulc a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.

5 Mwadyerera padziko, ndipo mwacita zokukondweretsani; mwadyetsa mitima yanu m'tsiku lakupha.

6 Munamtsutsa, munapha wolungamayo, iye sakanizainu.

Apirire, Za kulumbira, kupemphera kubweza wosocera

7 Potero, lezani mtima, abale, kufikira kudza kwace kwa Ambuye. Taonani, wolima munda alindira cipatso cofunikatu ca dziko, ndi kuleza mtima naco kufikira cikalandira mvula ya myundo ndi masika,

8 Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwace kwa Ambuye kuyandikira.

9 Musaipidwe wina ndi mnzace, abale, kuti mungaweruzidwe. Taonani, woweruza aima pakhomo.

10 Tengani, abale, citsanzo ca kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri ameneanalankhulam'dzina la Ambuyeo

11 Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za cipiriro ca Yobu, ndipo mwaona citsiriziro ca Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala cikondi, ndi wacifundo.

12 Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kuchula mwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina liri lonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akha; le iai; kuti mungagwe m'ciweruziro.

13 Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere, Kodi wina asekera? Ayimbire.

14 Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akuru a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye:

15 ndipo pemphero la cikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adacita macimo adzakhululukidwa kwa iye.

16 Cifukwa cace mubvomerezane wina ndi mnzace macimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzace kuti muciritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukuru m'macitidweace.

17 Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera cipempherere kuti isabvumbe mvula; ndipo, siinagwa mvula pa dzikozaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi.

18 Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zace.

19 Abale anga, ngati wina wa inu asocera posiyana ndi coonadi, ndipo ambweza iye mnzace;

20 azindikire, kuti iyeamene abweza wocimwa ku njira yace yosocera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzabvundikira macimo aunyinji.

Mitu

1 2 3 4 5