1 YAKOBO, kapolo wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Kristu, kwa mafuko khumi ndi awiri a m'cibalaliko: ndikulankhulani.
2 Muciyese cimwemwe cokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundu mitundu;
3 pozindikira kuti ciyesedwe ca cikhulupiriro canu cicita cipiriro.
4 Koma cipiriro cikhale nayo nchito yace yangwiro, kuti mukakhale angwiro ndi opanda cirema, osasowa kanthu konse.
5 Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye,
6 Koma apemphe ndi cikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi pfunde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.
7 Pakuti asayese munthu uyu kuti adzalandira kanthu kwa Ambuye;
8 munthu wa mitima iwiri akhala wosinkhasinkha pa njira zace zonse.
9 Koma mbale woluluka adzitamandire pa ukulu wace;
10 pakuti adzapita monga duwa la udzu,
11 Pakuti laturuka dzuwa ndi kutentha kwace, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lace, ndi ukoma wa maonekedwe ace waonongeka; koteronso wacuma adzafota m'mayendedwe ace.
12 Wodala munthu wakupirira poyesedwa; pakuti pamene wabvomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjezera iwo akumkonda iye.
13 Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo iye mwini sayesa munthu:
14 koma munthu ali yense ayesedwa pamene cilakolako cace ca iye mwini cimkokera, nicimnyenga.
15 Pamenepo cilakolakoco citaima, cibala ucimo; ndipo ucimo, utakula msinkhu, ubala imfa.
16 Musanyengedwe, abale anga okondedwa.
17 Mphatso iri yonse yabwino, ndi cininkho ciri conse cangwiro zicokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe cisanduliko, kapena mthunzi wa citembenukiro.
18 Mwa cifuniro cace mwini anatibala ife ndi mau a coonadi, kuti tikhale ife ngati zipatso zoundukula za zolengedwa zace.
19 Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu ali yense akhale wochera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.
20 Pakuti mkwiyo wa munthu sucita cilungamo ca Mulungu.
21 Mwa ici, mutabvula cinyanso conse ndi cisefukiro ca coipa, landirani ndi cifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.
22 Khalani akucita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.
23 Pakuti ngati munthu ali wakumva mau wosati wakucita, iyeyu afanana ndi munthu wakuyang'anira nkhope yace ya cibadwidwe cace m'kalirole;
24 pakuti wadziyang'anira yekha nacoka, naiwala pompaja nali wotani.
25 Koma iye wakupenyerera m'lamulo langwiro, ndilo laufulu, natero cipenyerere, ameneyo, posakhala wakumva wakuiwala, komatu wakucita nchito, adzakhala wodala m'kucita kwace.
26 Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lace, koma adzinyenga mtima wace, kupembedza kwace kwa munthuyu nkopanda pace.
27 Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: z kuceza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m'cisautso cao, ndi 1 kudzisungira mwini wosacitidwa mawanga ndi dziko lapansi.