Yakobo 3 BL92

Aziceniera ndi pakamwa pao

1 Musakhale aphunzitsi ambiri, abale anga, podziwa kuti tidzalangika koposa.

2 Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.

3 Koma ngati tiikiraakavalo zogwirira m'kamwa mwao atimvere, tipotolozanso thupi lao Ionse,

4 Taonani, zombonso, zingakhale zazikuru zotere, nizitengedwa ndi mphepo zolimba, zipotozeka ndi tsigiro laling'ono ndithu kumene kuli konse afuna wogwira tsigiro.

5 Kotero lilimenso liri ciwalo cacing'ono, ndipo lidzikuzira zazikuru, Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri!

6 Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la cosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a cibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi gehena.

7 Pakuti mtundu uli wonse wa nyama ndi wa mbalamenso, wa zokwawa, ndi wa zam'nyanja, zimazoloweretsedwa, ndipo zazoloweretsedwa ndi anthu;

8 koma lilime palibe munthu akhoza kulizoloweretsa; liri coipa cotakataka, lodzala ndi ululu wakupha.

9 Timayamika Ambuye ndi Atate nalo; nalonso timatemberera anthu, okhala monga mwa mafanizidwe a Mulungu;

10 mocokera m'kamwa momwemo muturuka ciyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.

11 Kodi kasupe aturutsira pa una womwewo madzi okoma ndi owawa?

12 Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amcere sakhoza kuturutsa okoma.

Nzeru yocokera Kumwamba

13 Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ace abwino nchito zace mu nzeru yofatsa.

14 Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi cotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana naco coonadi.

15 Nzeru iyi, sindiyo yotsika kumwamba, komatu iri ya padziko, ya cifuniro ca cibadwidwe, ya ziwanda.

16 Pakuti pomwe pali kaduka ndi zotetana, pamenepo pali cisokonekero ndi cocita coipa ciri conse.

17 Koma nzeru yocokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala cifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.

18 Ndipo cipatso ca cilungamo cifesedwa mumtendere kwa iwo akucita mtendere.

Mitu

1 2 3 4 5