Yakobo 2 BL92

Asacite tsankhu pakati pa anthu

1 Abate anga, musakhale naco cikhulupiriro ca Ambuye wathu Yesu Kristu, Ambuye wa ulemerero, ndi kusamala maonekedwe.

2 Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wobvala mphete yagolidi, ndi cobvala cokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi cobvala codetsa:

3 ndipo mukapenyerera iye wobvala cokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, ima uko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga;

4 kodi simunasiyanitsa mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?

5 Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankha osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi cikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonieza kwa iwo akumkonda iye?

6 Koma inu mumanyoza munthu wosauka. Kodi sakusautsani inu acuma, nakukokerani iwowa ku mabwalo a mirandu?

7 Kodi sacitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?

8 Koma ngati mucita cikwanirire lamulolo lacifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, mucita bwino:

9 koma ngati musamala maonekedwe, mucita ucimo, ndipo mutsutsidwa ndi cilamulo monga olakwa.

10 Pakuti amene ali yense angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wacimwira onse.

11 Pakuti Iye wakuti, Usacite cigololo, anatinso, Usaphe. Ndipo ukapanda kucita cigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo.

12 Lankhulani motero, ndipo citani motero, monga anthu amene adzaweruzidwa ndi lamulo la ufulu.

13 Pakuti ciweruziro ciribe cifundo kwa iye amene sanacita cifundo; cifundo cidzitamandira kutsutsana naco ciweruziro.

Cikhulupiriro copanda nchito zace cikhala copanda pace

14 Cipindulocace nciani, abale anga, munthu akanena, Ndiri naco cikhulupiriro, koma alibe nchito? Kodi cikhulupiriroco cikhoza kumpulumutsa?

15 Mbale kapena mlongo akakbalawausiwa, nieikamsowa cakudya ca tsiku lace,

16 ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, muitapfunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwace nciani?

17 Momwemonso cikhulupiriro, cikapanda kukhala nazo nchito, cikhala cakufa m'kati mwacemo.

18 Koma wina akati, Iwe uli naco cikhulupiriro, ndipo ine ndiri nazo nchito; undionetse ine cikhulupiriro cako copanda nchito zako, ndipo ine ndidzakuonetsa iweeikhulupiriro canga coturuka m'nchito zanga.

19 Ukhulupirira iwe kuti Mulungu ali mmodzi; ucita bwino; ziwanda zikhulupiranso, ndipo zinthunthumira.

20 Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pace iwe, kuti cikhulupiriro copanda nchito ciri cabe?

21 Abrabamu kholo lathu, sanayesedwa wolungama ndi nchito kodi, paja adapereka mwana wace Isake nsembe pa guwa la nsembe?

22 Upenya kuti cikhulupiriro cidacita pamodzi ndi nchito zace, ndipo moturuka mwa nchito cikhulupiriro cidayesedwa cangwiro;

23 ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye cilungamo; ndipo anachedwa bwenzi la Mulungu.

24 Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi nchito yace, osati ndi cikhulupiriro cokha.

25 Ndipo momwemonso sanayesedwa wolungama Rahabi mkazi wa damayo ndi nchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawaturutsa adzere njira yina?

26 Pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso cikhulupiriro copanda nchito ciri cakufa.

Mitu

1 2 3 4 5