2 kuti mukumbukile mau onenedwa kale ndi aneneri oyera, ndi lamulo la Ambuye ndi Mpulumutsi, mwa atumwi anu;
3 ndi kuyamba kucizindikira ici kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kucita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,
4 ndi kunena, Liri kuti lonjezano la kudza kwace? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga ciyambire cilengedwe.
5 Pakuti ici aiwala dala, kuti miyamba inakhala kale lomwe, ndi dziko lidaungika ndi madzi ndi mwa madzi, pa mau a Mulungu;
6 mwa izi dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidaonongeka;
7 koma miyamba ndi dziko lamasiku ano, ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira tsiku la ciweruzo ndi cionongeko ca anthu osapembedza.
8 Koma ici cimodzi musaiwale, okondedwa inu, kuti tsiku limodzi likhala kwa Ambuye ngati zaka cikwi, ndi zaka cikwi ngati tsiku limodzi.