1 PAULO a mtumwi wa Kristu Yesu mwa cifuniro ca Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Kristu Yesu,
2 kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Ambuye wathu.
3 Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi cikumbu mtima coyera, kuti ndikumbukila iwe kosalekeza m'mapemphero anga,
4 pokhumba usiku ndi usana kukuona iwe, ndi kukumbukila misozi yako, kuti ndidzazidwe naco cimwemwe;