1 Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu ndi Kristu Yesu, amene adzaweruza amoyo ndi akufa, ndi pa maonekedwe ace ndi ufumu wace;
2 lalikira mau; cita nao pa nthawi yace, popanda nthawi yace; tsutsa, dzudzula, cenjeza, ndi kuleza mtima konse ndi ciphunzitso.
3 Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola ciphunzitso colamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziuniikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:
4 ndipo adzalubza dala pacoonadi, nadzapatukira kutsata nthanu zacabe.
5 Koma iwe, khala maso m'zonse, imva zowawa, cita nchito ya mlaliki wa Uthenga Wabwino, kwaniritsa utumiki wako.
6 Pakuti ndirimkuthiridwa nsembe tsopano, ndipo nthawi ya kumasuka kwanga yafika.
7 Ndalimbana nako kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga cikhulupiriro:
8 cotsalira wandiikira ine korona wa cilungamo, amene Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa ine tsiku lijalo: ndipo si kwa ine ndekha, komatunso kwa onse amene anakonda maonekedwe ace.
9 Tayesetsa kudza kwa ine msanga:
10 pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalimatiya.
11 Luka yekha ali pamodzi ndi ine. Umtenge Marko, adze pamodzi ndi iwe; pakuti ayenera kunditumikira.
12 Koma Tukiko ndamtuma ku Efeso.
13 Copfunda cija ndinacisiya ku Trowa kwa Karpo, udze naco pakudza iwe, ndi mabuku, makamaka zikopa zija zolembedwa.
14 Alesandro wosula mkuwa anandicitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa nchito zace;
15 ameneyo iwenso ucenjere naye; pakuti anatsutsana nao mau athu.
16 Pa codzikanira canga coyamba panalibe mmodzi anandithangata, koma onse anandisiya; cimeneco cisawerengedwe cowatsutsa.
17 Koma Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine cilalikiro cimveke konse konse, ndi amitundu onse amve; ndipo ndinalanditsidwa m'kamwa mwa mkango.
18 Ambuye adzandilanditsa ku nchito yonse yoipa, nadzandipulumutsa ine kulowa Ufumu wace wa Kumwamba; kwa iye ukhale ulemerero ku nthawi za nthawi. Amen.
19 Lankhula Priska ndi Akula, ndi banja la Onesiforo.
20 Erasto anakhalira m'Korinto; koma Trofimo ndamsiya wodwala ku Mileto.
21 1 Tayesetsa kudza isanadze nyengo yacisanu. Akulankhula iwe Eubulo, ndi Pude, ndi Lino, ndi Klaudiya, ndi abale onse.
22 2 Ambuye akhale ndi mzimu wako. Cisomo cikhale nanu.