Tito 1 BL92

1 PAULO, kapolo wa Mulungu ndi mtumwi wa Yesu Kristu monga mwa cikhulupiriro ca osa nkhika a Mulungu, ndi cizindikiritso ca coonadi ciri monga mwa cipembedzo,

2 m'ciyembekezo ca moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;

3 koma pa nyengo za iye yekha anaonetsa mau ace muulalikiro, umene anandisungitsa ine, monga mwa lamulo la Mpulumutsi wathu Mulungu:

4 kwa Tito, mwana wanga weni weni monga mwa cikhulupiriro ca ife tonse: Cisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Mpulumutsi wathu.

Asenzetsa Tito udindo wakusunga Mpingo wa ku Krete. Atsutsa aphunzitsi onyenga

5 Cifukwa ca ici ndinakusiya iwe m'Krete, kuti ukalongosole zosowa, nukaike akuru m'midzi yonse, monga ndinakulamulira;

6 ngati wina ali wopanda cirema, mwamuna wa mkazi mmodzi, wokhala nao ana okhulupirira, wosasakaza zace, kapena wosakana kumvera mau.

7 Pakuti woyang'anira ayenera kukhala wopanda cirema, ngati mdindo wa Mulungu; wosati waliuma, wosapsa mtima msanga, wosati waciwawa, wopanda ndeu, wosati wa cisiriro conyansa;

8 komatu wokonda kucereza alendo, wokonda zokoma, wodziweruza, wolungama, woyera mtima, wodziletsa;

9 wogwira mau okhulupirika monga mwa ciphunzitso, kuti akakhoze kucenjeza m'ciphunzitso colamitsa, ndi kutsutsa otsutsana naye.

10 Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pace, ndi onyenga, makamaka iwo a kumdulidwe,

11 amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera cifukwa ca cisiriro conyansa.

12 Wina wa mwa iwo, ndiye mneneri wa iwo okha, anati, Akrete ndiwo amabodza masiku onse, zirombo zoipa, aumbombo, aulesi.

13 Umboni uwu uli woona. Mwa ici uwadzudzule mokaripa, kuti akakhale olama m'cikhulupiriro,

14 osasamala nthanu zacabe za Ciyuda, ndi malamulo a anthu opatuka kusiyana naco coonadi.

15 Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi cikumbu mtima cao.

16 Abvomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi Debito zao amkana iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa nchito zonse zabwino osatsimikizidwa.

Mitu

1 2 3