2 Timoteo 3 BL92

Zoipa zoopsa masiku otsiriza

1 Koma zindikira ici, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa.

2 Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndarama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,

3 osayera mtima, opanda cikondi cacibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino,

4 aciwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu;

5 akukhala nao maonekedwe a cipembedzo, koma mphamvu yace adaikana; kwa iwonso udzipatule,

6 Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundu mitundu:

7 ophunzira nthawi zonse, koma sakhoza konse kufikira ku cizindikiritso ca coonadi.

8 Ndipo monga momwe Yane ndi Yambre anatsutsana naye Mose, kotero iwonso atsutsana naco coonadi; ndiwo anthu obvunditsitsa mtima, osatsimikizidwa pacikhulupiriro.

9 Koma sadzapitirirapo; pakuti kupusa kwao kudzaonekeratu kwa onse, monganso kupusa kwa iwo aja.

Timoteo alimbike kutsata ziphunzitso zokoma, ndi kulalikira nthawi zonse

10 Koma iwe watsatatsata ciphunzitso canga, mayendedwe, citsimikizo mtima, cikhulupiriro, kuleza mtima, cikondi, cipiriro,

11 mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandicitira m'Antiokeya, m'Ikoniya, m'Lustro, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa.

12 Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.

13 Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa ciipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.

14 Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa;

15 ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira cipulumutso, mwa cikhulupiriro ca mwa Kristu Yesu.

16 Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m'cilungamo:

17 kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kucita nchito iri yonse yabwino.

Mitu

1 2 3 4