2 Timoteo 1 BL92

1 PAULO a mtumwi wa Kristu Yesu mwa cifuniro ca Mulungu, monga mwa lonjezano la moyo wa m'Kristu Yesu,

2 kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Ambuye wathu.

Cikondi ca Paulo ca pa Timoteo

3 Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi cikumbu mtima coyera, kuti ndikumbukila iwe kosalekeza m'mapemphero anga,

4 pokhumba usiku ndi usana kukuona iwe, ndi kukumbukila misozi yako, kuti ndidzazidwe naco cimwemwe;

5 pokumbukila cikhulupiriro cosanyenga ciri mwa iwe, cimene cinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mai wako Yunike, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.

6 Cifukwa cace ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, iri mwa iwe mwa kuika kwa manja anga,

7 Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi cikondi ndi cidziletso.

8 Potero usacite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wace; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;

9 amene anatipulumutsa ife, natiitana ife ndi maitanidwe oyera, si monga mwa nchito zathu, komatu monga mwa citsimikizo mtima ca iye yekha, ndi cisomo, copatsika kwa ife mwa Kristu Yesu zisanayambe nthawi zoyamba,

10 koma caonetsedwa tsopano m'maonekedwe a Mpulumutsi wathu Kristu Yesu, amenedi anatha imfa, naonetsera poyera moyo ndi cosabvunda mwa Uthenga Wabwino,

11 umene ndaikikapo mlaliki, ndi mtumwi ndi mphunzitsi wace.

12 Cifukwa ca ideo ndinamva zowawa izi; komatu sindicita manyazi; pakuti ndimdziwa iye amene ndamkhulupirira, ndipo ndikopeka mtima kuti ali wa mphamvu ya kudikira cosungitsa eangaeo kufikira tsiku lijalo.

13 Gwira citsanzo ca mau a moyo, amene udawamva kwa ine, mwa cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.

14 Cosungitsa cokomaca udikire mwa Mzimu Woyera amene akhalitsa mwa ife.

15 Ici ucidziwa, kuti onse a m'Asiya adabwerera kusiyana nane; a iwo ali Fugelo ndi Hermogene,

16 Ambuye acitire banja la Onesiforo cifundo; pakuti anatsitsimutsa ine kawiri kawiri, ndipo sanacita manyazi ndi unyolo wanga;

17 komatu pokhala m'Roma iye anandifunafuna ine ndi khama, nandipeza,

18 (Ambuye ampatse iye apeze cifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri m'Efeso, uzindikira iwe bwino.

Mitu

1 2 3 4