2 kwa Timoteo, mwana wanga wokondedwa: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Kristu Yesu Ambuye wathu.
3 Ndiyamika Mulungu, amene ndimtumikira kuyambira makolo anga ndi cikumbu mtima coyera, kuti ndikumbukila iwe kosalekeza m'mapemphero anga,
4 pokhumba usiku ndi usana kukuona iwe, ndi kukumbukila misozi yako, kuti ndidzazidwe naco cimwemwe;
5 pokumbukila cikhulupiriro cosanyenga ciri mwa iwe, cimene cinayamba kukhala mwa mbuye wako Loisi, ndi mwa mai wako Yunike, ndipo, ndakopeka mtima, mwa iwenso.
6 Cifukwa cace ndikukumbutsa iwe ukoleze mphatso ya Mulungu, iri mwa iwe mwa kuika kwa manja anga,
7 Pakuti Mulungu sanatipatsa mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi cikondi ndi cidziletso.
8 Potero usacite manyazi pa umboni wa Ambuye wathu, kapena pa ine wandende wace; komatu umve masautso ndi Uthenga Wabwino, monga mwa mphamvu ya Mulungu;