1 Ndipo iwe, mwana wanga, limbika m'cisomo ca m'Kristu Yesu.
2 Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.
3 Umve zowawa pamodzi nane monga msilikari wabwino wa Kristu Yesu.
4 Msilikari sakodwa nazo nchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikari.
5 Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani a masewero, sambveka korona ngati sanayesana monga adapangana.
6 Wam'munda wogwiritsitsa nchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozoo