2 Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.
3 Umve zowawa pamodzi nane monga msilikari wabwino wa Kristu Yesu.
4 Msilikari sakodwa nazo nchito wamba, kuti akakondweretse iye amene adamlemba usilikari.
5 Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani a masewero, sambveka korona ngati sanayesana monga adapangana.
6 Wam'munda wogwiritsitsa nchitoyo ayenera akhale woyamba kulandira zipatsozoo
7 Lingirira cimene ndinena; pakuti Ambuye adzakupatsa cidziwitso m'zonse.
8 Kumbukila Yesu Kristu, wouka kwa akufa, wocokera m'mbeu ya Davide, monga mwa Uthenga Wabwino wanga;