1 PAULO ndi Timoteo, akapolo a Yesu Kristu, kwa oyera mtima onse mwa Kristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:
2 Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.
3 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;
4 nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndicita pembedzerolo ndi kukondwera,
5 cifukwa ca ciyanjano canu cakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;
6 pokhulupira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu nchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Kristu;
7 monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndiri nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'codzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'cisomo.