Afilipi 3 BL92

A wacenjeza asatsate alum wi onyenga, Aonetsere zipatso za Mzimu

1 Cotsalira, abale anga, kondwerani mwa Ambuye. Kulembera zomwezo kwa inu, sikundibvuta ine, koma kwa inu kuli kukhazikitsa.

2 Penyererani agaru, penyererani ocita zoipa, penyererani coduladula;

3 pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Yesu Kristu, osakhulupirira m'thupi;

4 ndingakhale inenso ndiri nako kakukhulupirira m'thupi; ngati wina yense ayesa kukhulupirira m'thupi, makamaka ineyu;

5 wodulidwa tsiku lacisanu ndi citatu, wa mbadwo wa Israyeli, wa pfuko la Benjamini, Mhebri wa mwa Ahebri; monga mwa lamulo, Mfarisi;

6 monga mwa cangu, wolondalonda Eklesia; monga mwa cilungamo ca m'lamulo wokhala wosalakwa ine.

7 Komatu zonse zimene zinandipindulira, zomwezo ndinaziyesa citayiko cifukwa ca Kristu.

8 Komatu zeni zeninso ndiyesa zonse zikhale citayiko cifukwa ca mapambanidwe a cizindikiritso ca Kristu Yesu Ambuye wanga, cifukwa ca Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadzionjezere Kristu,

9 ndi kupezedwa mwa iye, wosati wakukhala naco cilungamo canga ca m'lamulo, koma cimene ca mwa cikhulupiriro ca Kristu, cilungamoco cocokera mwa Mulungu ndi cikhulupiriro;

10 kuti ndimzindikire iye, ndi mphamvu ya kuuka kwace, ndi ciyanjano ca zowawa zace, pofanizidwa ndi imfa yace;

11 ngati nkotheka ndikafikire kuuka kwa akufa.

12 Si kunena kuti ndinalandira kale, kapena kuti ndatha kukonzeka wamphumphu; koma ndilondetsa, ngatinso ndikacigwire ici cimene anandigwirira Yesu Kristu.

13 Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kucigwira: koma cinthu cimodzi ndicicita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo,

14 ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Kristu Yesu.

15 Tonsefe amene tsono tidakonzeka amphumphu, tilingirire ici mumtima; ndipo ngati kuli kanthu mulingirira nako kwina mumtima, akanso Mulungu adzabvumbulutsira inu;

16 cokhaci, kumene tidafikirako, mayendedwe athu alinganeko.

17 Abale khalani pamodzi akutsanza anga, ndipo yang'anirani iwo akuyenda kotero monga muli ndi ife citsanzo canu.

18 Pakuti ambiri amayenda, za amene ndinakuuzani kawiri kawiri, ndipo tsopanonso ndikuuzani ndi kulira, ali adani a mtanda wa Kristu;

19 citsiriziro cao ndico kuonongeka, mulungu wao ndiyo niimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amenealingirira za padziko.

20 Pakuti ufulu wathu uli Kumwamba; z kucokera komwenso tilindirira Mpulumutsi, Ambuye Yesu Kristu;

21 amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lace la ulemerero, monga mwa macitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse.

Mitu

1 2 3 4