Afilipi 2 BL92

1 Ngati tsono muli citonthozo mwa Kristu, ngati cikhazikitso ca cikondi, ngati ciyanjano ca Mzimu, ngati phamphu, ndi zisoni,

2 kwaniritsani cimwemwe canga, kuti mukalingalire mtima zomwezo, akukhala naco cikondi comwe, a moyo umodzi, olingalira mtima umodzi;

3 musacite kanthu monga mwa cotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pace, komatu ndi kudzicepetsa mtima, yense ayese anzace omposa iye mwini;

4 munthu yense asapenyerere zace za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzaceo

5 Mukhale nao mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Kristu Yesu,

6 ameneyo, pokhala nao maonekedwe a Mulungu, sanaciyesa colanda kukhala wofana ndi Mulungu,

7 koma anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe akapolo, nakhala m'mafanizidwe a anthu;

8 ndipo popezedwa m'maonekedwe ngati munthu, anadzicepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya pamtanda.

9 Mwa icinso Mulungu anamkwezetsa iye, nampatsa dzina limene liposa maina onse,

10 kuti m'dzina la Yesu bondo liri lonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko,

11 ndi malilime onse abvomere kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kucitira ulemu Mulungu Atate.

12 Potero, okondedwa anga, monga momwe mumvera nthawi zonse, posati pokha pokha pokhala ine ndiripo, komatu makamaka tsopano pokhala ine palibe, gwirani nchito yace ya cipulumutso canu ndi mantha, ndi kunthunthumira;

13 pakuti wakucita mwa inu kufuna ndi kucita komwe, cifukwa ca kukoma mtima kwace, ndiye Mulungu,

14 Citani zonse kopanda madandaulo ndi makani,

15 kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda cirema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,

16 akuonetsera mau a movo; kuti ine ndikakhale wakudzitamandira: nao m'tsiku la Kristu, kuti sindinathamanga cabe, kapena kugwiritsa nchito cabe.

17 Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa cikhulupiriro canu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;

18 momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.

Paulo atamula Timoteo ndi Epafrodito amithenga ace a kwa Afilipi

19 Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.

20 Pakuti ndiribe wina wa mtima womwewo, amene adza: samalira za kwa inu ndi mtima woona.

21 Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Kristu.

22 Koma muzindikira matsimikizidwe ace, kuti, monga mwana acitira atate wace, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.

23 Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posacedwa m'mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani;

24 koma ndikhulupirira mwa Ambuye kuti ine ndekhanso ndidzadza msanga.

25 Koma ndinayesa nkufunika kutuma kwa inu Epafrodito mbaleyo, ndiye wanchito mnzanga ndi msilikari mnzanga, ndiye mtumwi wanu, ndi wonditumikira pa cosowa canga;

26 popeza anali wolakalaka inu nonse, nabvutika mtima cifukwa mudamva kuti anadwala.

27 Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamcitira cifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale naco cisoni cionjezere-onjezere.

28 Cifukwa cace ndamtuma iye cifulumizire, kuti pakumuona mukakondwerenso, ndi inenso cindicepere cisoni.

29 Cifukwa cace mumlandire mwa Ambuye, ndi cimwemweconse; nimucitire ulemu oterewa;

30 pakuti cifukwa lea nchito ya Kristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wace, kuti z akakwaniritse ciperewero ca utumiki wanu wa kwa ine.

Mitu

1 2 3 4