Afilipi 1 BL92

1 PAULO ndi Timoteo, akapolo a Yesu Kristu, kwa oyera mtima onse mwa Kristu Yesu, akukhala ku Filipi, pamodzi ndi oyang'anira ndi atumiki:

2 Cisomo kwa inu ndi mtendere za kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Kristu.

Cikondi ca Paulo ca pa Afilipi; Zipatso za undende wace

3 Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse;

4 nthawi zonse m'pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndicita pembedzerolo ndi kukondwera,

5 cifukwa ca ciyanjano canu cakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;

6 pokhulupira pamenepo, kuti iye amene anayamba mwa inu nchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Kristu;

7 monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndiri nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'codzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'cisomo.

8 Pakuti Mulungu ali mboni yanga, kuti ndilakalaka inu nonse m'phamphu la mwa Kristu Yesu.

9 Ndipo ici ndipempha, kuti cikondi canu cisefukire cionjezere, m'cidziwitso, ndi kuzindikira konse;

10 kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Kristu;

11 odzala nacocipatso ca cilungamo cimene ciri mwa Yesu Kristu, kucitira Mulungu ulemerero ndi ciyamiko.

12 Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidacita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;

13 kotero kuti zomangira zanga zinaonekera mwa Kristu m'bwalo lonse da alonda, ndi kwa onse ena;

14 ndi kuti unyinji wa abale mwa Ambuye, pokhulupirira m'zomangira zanga, alimbika mtima koposa kulankhula mau a Mulungu opanda mantha.

15 Enatu alalikiranso Kristu cifukwa ca kaduka ndi ndeu; koma enanso cifukwa ca kukoma mtima;

16 ena atero ndi cikondi, podziwa kuti anandiika ndicite eokanira ca Uthenga Wabwino;

17 koma ena alalikira Kristu mocokera m'cotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira cisautso m'zomangira zanga.

18 Potero nciani? Cokhaco kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'coonadi, Kristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

19 Pakuti ndidziwa kuti ici cidzandicitira ine cipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Kristu;

20 monga mwa kulingiriritsa ndi ciyembekezo canga, kuti palibe cinthu cidzandicititsa manyazi, komatu mwa kulimbika mtima konse, monga nthawi yonse, tsopanonso Kristu adzakuzidwa m'thupi langa, kapena mwamoyo, kapena mwa imfa.

21 Pakuti kwa ine kukhala ndi moyo ndiko Kristu, ndi kufa kuli kupindula.

22 Koma ngati kukhala ndi moyo m'thupi, ndiko cipatso ca nchito yanga, sindizindikiranso cimene ndidzasankha.

23 Koma ndipanidwa nazo ziwirizi, pokhala naco colakalaka ca kucoka kukhala ndi Kristu, ndiko kwabwino koposa-posatu;

24 koma kukhalabe m'thupi ndiko kufunika koposa, cifukwa ca inu.

25 Ndipo pokhulupirira pamenepo ndidziwa kuti ndidzakhala, ndi kukhalitsa ndi inu nonse, kuonjezeracimwemwe ca cikhulupiriro canu;

26 kuti kudzitamandira kwanu kucuruke m'Kristu Yesu mwa ine, mwa kukhalanso ine kwa inu.

Akristu alimbike, ayanjane, adzicepetse, atsate kuyera-mtima

27 Cokhaci, mayendedwe anu ayenere Uthenga Wabwino wa Kristu: kuti, ndingakhale nditi ndirinkudza ndi kuona inu, ndingakhale nditi ndiri kwina, ndikamva za kwa inu, kuti mucirimika mu mzimu umodzi, ndi kugwirira pamodzi ndi moyo umodzi cikhulupiriro ca Uthenga Wabwino;

28 osaopa adani m'kanthu konse, cimene ciri kwa iwowa cisonyezo ca cionongeko, koma kwa inu ca cipulumutso, ndico ca kwa Mulungu;

29 kuti kwapatsidwa kwa inu kwaufulu cifukwa ca Kristu, si kukhulupirira kwa iye kokha, komatunso kumva zowawa cifukwa ca iye,

30 ndi kukhala naco inu cilimbano comweci mudaciona mwa ine, nimukumva tsopano ciri mwa ine.

Mitu

1 2 3 4