1 Ananu, mverani akukubalani mwa Ambuye, pakuti ici ncabwino.
2 Lemekeza atate wako ndi amako (ndilo lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano),
3 kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikuru padziko.
4 Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi cilangizo ca Ambuye.
5 Akapolo inu, mverani iwo amene ali ambuye anu monga mwa thupi, ndi kuwaopa ndi kunthunthumira nao, ndi mtima wanu wosakumbukila kanthu kena, monga kwa Kristu;
6 si monga mwa ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akucita cifuniro ca Mulungu cocokera kumtima;
7 akucita ukapolo ndi kubvomereza mtima, monga kutumikira Yesu Kristu, si anthu ai;
8 podziwa kuti cinthu cokoma ciri conse yense acicita, adzambwezera comweci Ambuye, angakhale ali kapolo kapena mfulu.
9 Ndipo, ambuye inu, muwacitire zomwezo iwowa, nimuleke kuwaopsa; podziwa kuti Ambuye wao ndi wanu ali m'Mwamba, ndipo palibe tsankhu kwa iye.
10 Cotsalira, tadzilimbikani mwa Ambuye, ndi m'kulimba kwa mphamvu yace.
11 Tabvalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kucirimika pokana macenjerero a mdierekezi.
12 Cifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akucita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi a uzimu a coipa m'zakumwamba.
13 Mwa ici mudzitengere zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoza kuima citsutsire pofika tsiku loipa, ndipo, mutacita zonse, mudzacirimika.
14 Cifukwa cace cirimikani, mutadzimangira m'cuuno mwanu ndi coonadi, mutabvalanso capacifuwa ca cilungamo;
15 ndipo mutadzibveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere;
16 koposa zonse mutadzitengeranso cikopa ca cikhulupiriro, cimene mudzakhoza kuzima naco mibvi yonse yoyaka moto ya woipayo.
17 Mutengenso cisoti ca cipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mau a Mulungu;
18 mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo poeezera pamenepo cicezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,
19 ndi ine ndemwe, kuti andipatse mau m'kunditsegulira m'kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu cinsinsico ca Uthenga Wabwino,
20 cifukwa ca umene 1 ndiri mtumiki wa m'unyolo, kuti m'menemo ndikalankhule molimbika, monga ndiyenera kulankhula.
21 Koma 2 kuti mukadziwe inunso za kwa ine, zimene ndicita, zinthu zonse adzakuzindikiritsani Tukiko mbale wokondedwayo, ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye;
22 amene ndamtuma kwa inu cifukwa ca icico, kuti mukazindikire za kwa ife, ndi kuti akatonthoze mitima yanu.
23 3 Mtendere ukhale kwa abale, ndi cikondi, pamodzi ndi cikhulupiriro, zocokera kwa Mulungu Atate, ndi Ambuye Yesu Kristu.
24 Akhale naco cisomo onse akukonda Ambuye wathu Yesu Kristu m'eosaonongeka.