Aefeso 5 BL92

1 Cifukwa cace khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa;

2 ndipo yendani m'cikondi monganso Kristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, copereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale pfungo lonunkhira bwino.

3 Koma dama ndi cidetso conse, kapena cisiriro, zisachulidwe ndi kuchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;

4 kapena cinyanso, ndi kulankhula zopanda pace, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka ciyamiko.

5 Pakuti ici mucidziwe kuti wadama yense, kapena wacidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe colowa m'ufumu wa Kristu ndi Mulungu.

6 Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pace, pakuti cifukwa ca hi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.

7 Cifukwa cace musakhale olandirana nao;

8 pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,

9 pakuti cipatso ca kuunika ticipeza m'ubwino wonse, ndi cilungamo, ndi coonadi,

10 kuyesera cokondweretsa Ambuye nciani;

11 ndipo musayanjane nazo nchito za mdima zosabala kanthu, koma maka-makanso muzitsutse;

12 pakuti zocitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kucititsa manyazi.

13 Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti conse cakuonetsa ciri kuunika.

14 Mwa ici anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndi, po Kristu adzawala pa iwe.

15 Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;

16 akucita macawi, popeza masiku ali oipa,

17 Cifukwa cace musakhale opusa, koma dziwitsani cifuniro ca Ambuye nciani.

18 Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli citayiko; komatu mudzale naye Mzimu,

19 ndi kudzilankhulira nokha ndi masalmo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira ndi kuyimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu;

20 ndi kuyamika Mulungu Atate masiku onse, cifukwa ca zonse, m'dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu;

21 ndi kumverana wina ndi mnzace m'kuopa Kristu.

Zoyenera m'banja la munthu

22 Akazi Inu, mverani amuna anu ainu eni, monga kumvera Ambuye.

23 Pakuti mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia, ali yekha Mpulumutsi wa thupilo.

24 Komatu monga Eklesia amvera Kristu, koteronso akazi amvere amuna ao m'zinthu zonse.

25 Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m'malo mwace;

26 kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;

27 kutilye akadziikire yekha Eklesia wa ulemerero, wopanda banga, kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda cirema.

28 Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;

29 pakuti munthu sanadana nalo thupi lace ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga, monganso Kristu Eklesia;

30 pakuti tiri ziwalo za thupi lace.

31 1 Cifukwa ca ici munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wace; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi.

32 Cinsinsi ici ncacikuru; koma ndinena ine za Kristu ndi Eklesia.

33 Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wace wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo 2 mkaziyo akumbukile kuti aziopa mwamuna.

Mitu

1 2 3 4 5 6