1 PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu, mwa cifuniro ca Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Kristu Yesu:
2 Cisomo kwa inu, ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Kristu.
3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Kristu;
4 monga anatisankha ife mwa iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda cirema pamaso pace m'cikondi,
5 Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana, a iye yekha mwa Yesu Kristu, monga umo kunakomera cifuniro cace,
6 kuti uyamikidwe ulemerero wa cisomo cace, cimene anaticitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.
7 Tiri ndi maomboledwe mwa mwazi wace, cikhululukiro ca zocimwa, monga mwa kulemera kwa cisomo cace,
8 cimene anaticurukitsira ife m'nzeru zonse, ndi cisamaliro.
9 Anatizindikiritsa ife cinsinsi ca cifuniro cace, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa iye,
10 kuti pa tnakonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Kristu, za kumwamba, ndi za padziko.
11 Mwa iye tinayesedwa colowa cace, popeza tinakonzekeratu monga mwa citsimikizo mtima ca iye wakucita zonse monga mwa uphungu wa cifuniro cace;
12 kuti ife amene dnakhulupirira Kristu kale tikayamikitse ulemerero wace.
13 Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a coonadi, Uthenga Wabwino wa cipulumutso canu; ndi kumkhulupirira iye, munasindikizidwa cizindikilo ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,
14 ndiye cikole ca colowa cathu, kuti ace ace akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wace uyamikike.
15 Mwa ici inenso, m'mene ndamva za cikhulupiriro'ca mwa Ambuye Yesu ciri mwa inu, cimenenso mufikitsira oyera mtima onse,
16 sindileka kuyamikacifukwa ca inu, ndi kukumbukila inu m'mapemphero anga;
17 kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa bvumbulutso kuti mukamzindikire iye;
18 ndiko kunena kuti maso amitima yanu awalitsike, ktiti mukadziwe inu ciyembekezo ca kuitana kwace nciani; cianinso cuma ca ulemerero wacolowa cace mwa oyera mtima,
19 ndi ciani ukuru woposa wa mphamvu yace ya kwa ife okhulupira, monga mwa macitidwe a mphamvu yace yolimba,
20 imene anacititsa mwa Kristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, 1 namkhazikitsa pa dzanja lace lamanja m'zakumwamba,
21 2 pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina liri lonse lochedwa, si m'nyengo yinoya pansi pano yokha, komanso mwaiyo ikudza;
22 ndipo 3 anakonza zonse pansi pa mapazi ace, nampatsa iye 4 akhale mutu pamtu pa zonse,
23 5 kwa Eklesia amene ali thupi lace, 6 mdzazidwe wa iye amene adzazazonse m'zonse.