Aefeso 4 BL92

Umodzi wa iwo a cikhulupiriro

1 Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,

2 ndi kuonetsera kudzicepetsa konse, ndi cifatso, ndi kuonetsera cipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzace, mwa cikondi;

3 ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa cimangiriro ca mtendere.

4 Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'ciyembekezo cimodzi ca maitanidwe anu;

5 Ambuye mmodzi, cikhulupiriro cimodzi, ubatizo umodzi,

6 Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.

7 Ndipo kwa yense wa ife capatsika cisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Kristu.

8 Cifukwa cace anena,M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende,Naninkha zaufulu kwa anthu.

9 Koma ici, cakuti, Anakwera, nciani nanga komakuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?

10 Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.

11 Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi enaaneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;

12 kuti akonzere oyera mtima: ku nchito ya utumiki, kumangirira thupi la Kristu;

13 kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa cikhulupiriro, ndi wa cizindikiritso ca Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa cidzaloca Kristu.

14 Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengeka-tengeka ndi mphepo yonse ya ciphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kucenjerera kukatsata cinyengo ca kusoceretsa;

15 koma ndi kucita zoona mwa cikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira iye amene ali mutu ndiye Kristu;

16 kucokera mwa Iye thupi lonse, lokowanidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kucititsa kwa ciwalo conse pa muyeso wace, licita makulidwe a thupi, kufikira cimango cace mwa cikondi.

Kusiyana kwa kuyera mtima kwa Cikristu ndi mayendedwe oipa a akunja

17 Pamenepo ndinena ici, ndipo ndicita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'citsiru ca mtima wao,

18 odetsedwam'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, cifukwa ca cipulukiro ciri mwa iwo, cifukwa ca kuumitsa kwa mitima yao;

19 amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti acite cidetso conse mu umbombo.

20 Koma inusimunaphunzira Kristu cotero,

21 ngatitu mudamva iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa iye, monga coonadi ciri mwa Yesu;

22 kuti mubvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wobvunda potsata zilakolako za cinyengo;

23 koma kuti 1 mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,

24 2 nimubvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'cilungamo, ndi m'ciyero ca coonadi.

25 Mwa ici, mutataya zonama, 3 lankhulani zoona yense ndi mnzace; 4 pakuti tiri ziwalo wina ndi mnzace.

26 5 Kwiyani, koma musacimwe; dzuwa lisalowe muli cikwiyire,

27 ndiponso 6 musampatse malo mdierekezi.

28 Wakubayo asabenso; koma 7 makamaka agwiritse nchito, nagwire nchito yokoma ndi manja ace, kuti akhale naco cakucereza wosowa.

29 8 Nkhani yonse yobvunda isaturuke m'kamwa mwanu, koma ngati pali yina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, 9 kuti ipatse cisomo kwa iwo akumva.

30 Ndipo 10 musamvetse cisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa cizindikilo mwa iye, kufikira tsiku la maomboledwe.

31 11 Ciwawo conse, ndi kupsya mtima, ndi mkwiyo, ndi ciwawa, ndi mwano zicotsedwe kwa inu, ndiponso coipa conse.

32 Koma 12 mukhalirane okoma wina ndi mnzace, a mtima wacifundo, akukhululukirana nokha, 13 monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.

Mitu

1 2 3 4 5 6