Aefeso 3 BL92

Cinsinsi ca maitanidwe a amitundu

1 Cifukwa ca ici ine Paulo, ndine wandende wa Kristu Yesu cifukwa ca inu amitundu,

2 ngatitu munamva za udindo wa cisomo ca Mulungucimene anandipatsa ine ca kwa inu;

3 ndi umo anandizindikiritsa cinsinsico mwa bvumbulutso, monga ndinalemba kale mwacidule,

4 cimene mukhoza kuzindikira naco, pakuciwerenga, cidziwitso canga m'cinsinsi ca Kristu,

5 cimene sanacizindikiritsa ana a anthu m'mibadwo yina, monga anacibvumbulutsa tsopano kwa atumwi ndi aneneri ace oyera mwa Mzimu,

6 kuti amitundu ali olowanyumbapamodzi ndi ife, ndi ziwalo zinzathu za thupilo, ndi oland ira nafe pamodzi palonjezano mwa Kristu Yesu, mwa Uthenga Wabino,

7 umene anandikhalitsa mtumiki wace monga mwa mphatso ya cisomo ca Mulungu, cimene anandipatsa ine, monga mwa, macitidwe a mphamvu yace.

8 Kwa ine wocepa ndi wocepetsa wa onse, oyera mtima anandipatsa cisomo ici, ndilalikire kwa amitundu cuma cosalondoleka ca Kristu;

9 ndi kuwalitsira onse adziwe makonzedwe a cinsinsico, cimene cinabisika ku yambira kale kale mwa Mulungu wolenga zonse;

10 kuti mu Eklesia azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu,

11 monga mwa citsimikizo mtima ca nthawi za nthawi, cimene anacita mwa Kristu Yesu Ambuye wathu:

12 amene tiri naye cokhazikika mtima ndi ciyandiko eolimbika, mwa cikhulupiriro ca pa iye.

13 Mwa ici ndipempha kuti musade mtima, m'zisautso zanga cifukwa ca inu, ndiwo ulemerero wanu.

Paulo apempherera Aefeso

14 Cifukwa ca ici ndipinda maondo anga kwa Atate,

15 amene kucokera kwa iye pfuko lonse la m'mwamba ndi la padziko alicha dzina,

16 kuti monga mwa cuma ca ulemerero wace akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wace, m'kati mwanu,

17 kuti Kristu akhale cikhalire mwa cikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'cikondi,

18 mukakhozetu kuzindikira pamodzi ndi oyera mtima onse, kupingasa, ndi utali, ndi kukwera,

19 ndi kuzama nciani; ndi kuzindikira cikondi ca Kristu, cakuposa mazindikiridwe, kuti mukadzazidwe kufikira cidzalo conse ca Mulungu.

20 Ndipo kwa iye amene angathe kucita koposa-posatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kucita mwa ife,

21 kwa iye ukhale ulemerero mu Mpingo ndi mwa Kristu Yesu, kufikira mibadwo yonse ya nthawi za nthawi. Amen.

Mitu

1 2 3 4 5 6