17 Komatu ngatinso ndithiridwa pa nsembe ndi kutumikira kwa cikhulupiriro canu, ndikondwera, ndipo ndikondwera pamodzi ndi inu nonse;
18 momwemonso kondwerani inu, nimukondwere pamodzi ndi ine.
19 Koma ndiyembekeza mwa Ambuye Yesu kuti ndidzatumiza Timoteo kwa inu msanga, kuti inenso nditonthozeke bwino pozindikira za kwa inu.
20 Pakuti ndiribe wina wa mtima womwewo, amene adza: samalira za kwa inu ndi mtima woona.
21 Pakuti onsewa atsata za iwo okha, si za Yesu Kristu.
22 Koma muzindikira matsimikizidwe ace, kuti, monga mwana acitira atate wace, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.
23 Ameneyo ndithu tsono ndiyembekeza kumtuma posacedwa m'mene ndikapenyerera za kwa ine zidzatani;