1 Potero, abale anga okondedwa, olakalakidwa, ndinu cimwemwe canga ndikorona wanga, cirimikani motere mwa Ambuye, okondedwa.
2 Ndidandaulira Euodiya, ndidandaulira Suntuke, alingirire ndi mtima umodzi mwa Ambuye.
3 Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klementonso, ndi otsala aja anchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la moyo.
4 Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.
5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.