1 PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu mwa cifuniro ca Mulungu, ndi Timoteo mbaleyo,
2 kwa oyera mtima ndi abale okhulupirika mwa Kristu a m'Kolose: Cisomo kwa inu ndi mtendere wocokera kwa Mulungu Atate wathu.
3 Tiyamika Mulungu Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu ndi kupempherera Inu nthawi zonse,
4 popeza tidamva za cikhulupiriro canu ca mwa Kristu Yesu, ndi cikondi muli naco kwa oyera mtima onse;
5 cifukwa ca ciyembekezo cosungikira kwa inu m'Mwamba, cimene mudacimva kale m'mau a coonadi ca Uthenga Wabwino,
6 umene udafikira kwa inu; monganso m'dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula, monganso mwa inu; kuyambira tsikulo mudamva nimunazindildra cisomo ca Mulungu m'coonadi;