13 amene anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa cikondi cace;
14 amene tiri nao maomboledwe mwa iye, m'kukhululukidwa kwa zocimwa zathu;
15 amene ali fanizo la Mulungu wosaonekayo, wobadwa woyamba wa cilengedwe conse;
16 pakuti mwa iye, zinalengedwa zonse za m'mwamba, ndi za padziko, zooneka ndi zosaonekazo, kapena mipando yacifumu, kapena maufumu, kapena maukulu, kapena maulamuliro; zinthu zonse zinalengedwa mwa iye ndi kwa iye.
17 Ndipo iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye.
18 Ndipo iye ali mutu wa thupi, Eklesiayo; ndiye ciyambi, wobadwa woyamba woturuka mwa akufa; kuti akakhale iye mwa zonse woyambayamba.
19 Pakuti kunamkomera Atate kuti mwa iye cidzalo conse cikhalire,