20 mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, atacita mtendere mwa mwazi wa mtanda wace; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'mwamba.
21 Ndipo inu, okhala alendo kale ndi adani m'cifuwa canu m'nchito zoipazo, koma tsopano anakuyanjanitsani
22 m'thupi lace mwa imfayo, kukaimika inu oyera, ndi opanda cirema ndi osatsutsika pamaso pace;
23 ngatitu mukhalabe m'cikhulupiriro, ocirimika ndi okhazikika ndi osasunthika kulekana naco ciyembekezo ca Uthenga Wabwino umene mudaumva, wolalikidwa colengedwa conse ca pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wace.
24 Tsopano 1 ndikondwera nazo zowawazo cifukwa ca inu, ndipo 2 ndikwaniritsa zoperewera za cisautso ca Kristu m'thupi langa 3 cifukwa ca thupi lace, ndilo Eklesiayo;
25 amene ndinakhala mtumiki wace, 4 monga mwa udindo wa Mulungu umene anandipatsa ine wakucitira inti, wakukwaniritsa mau a Mulungu,
26 5 ndiwo cinsinsico cinabisika kuyambira pa nthawizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo; koma anacionetsa tsopano kwa oyera mtima ace,