7 monga momwe munaphunzira kwa Epafra kapolo mnzathu wokondedwa, ndiyemtumiki wokhulupirika wa Kristu cifukwa ca ife;
8 amenenso anatifotokozera cikondi canu mwa Mzimu.
9 Mwa ici ifenso, kuyambira tsiku limene tidamva, sitileka kupembedzera ndi kupempherera inu, kuti mukadzazidwe ndi cizindikiritso ca cifuniro cace mu nzeru zonse ndi cidziwitso ca mzimu,
10 kuti mukayende koyenera Ambuye kukamkondweretsa monsemo, ndi kubala zipatso mu nchito yonse yabwino, ndi kukula m'cizindikiritso ca Mulungu;
11 olimbikitsidwa m'cilimbiko conse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wace, kucitira cipiriro conse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi cimwemwe,
12 ndi kuyamika Atate, amene anatiyeneretsa ife kulandirana nao colowa ca oyera mtima m'kuunika;
13 amene anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa m'ufumu wa Mwana wa cikondi cace;