1 Pakuti ndifuna kuti inu mudziwe nkhawa imene ndiri nayo cifukwa ca inu, ndi iwowa a m'Laodikaya, ndi onse amene sanaone nkhope yanga m'thupi;
2 kuti itonthozeke mitima yao, nalumikizike pamodzi iwo m'cikondi, kufikira cuma conse ca cidzalo ca cidziwitso, kuti akazindikire Iwo cinsinsi ca Mulungu, ndiye Kristu,
3 amene zolemera zonseza nzeru ndi cidziwitso zibisika mwa iye.
4 Ici ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa.
5 Pakuti ndingakhale ndiri kwina m'thupi, komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi cilimbiko ca cikhulupiriro canu ca kwa Kristu.
6 Cifukwa cace monga momwe munalandira Kristu Yesu Ambuye, muyende mwa iye,