19 kucokera kwa iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempa, likula ndi makulidwe a Mulungu.
20 Ngati munafa pamodzi ndi Kristu kusiyana nazo zoyambaza dziko lapansi, mugonieranii ku zoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m'dziko lapansi,
21 usaikapo dzanja, usalawa, usakhudza,
22 (ndizo zonse zakuonongedwa pocita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?
23 zimene ziri naotu manenedwe a nzeru m'kutumikira kwa cifuniro ca mwini wace, ndi kudzicepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma ziribe mphamvu konse yakuletsa cikhutitso ca thupi.