1 Cifukwa cace ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Kristu, funani zakumwamba, kumene kuli Kristu wokhala pa dzanja lamanja la Mulungu.
2 Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.
3 Pakuti munafa, ndipo moyo wanu wabisika pamodzi ndi Kristu mwa Mulungu,
4 Pamene Kristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.
5 Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;
6 cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;
7 zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,