13 kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
14 koma koposa izi zonse khalani naco cikondano, ndico comangira ca mtima wamphumphu.
15 Ndipo mtendere wa Kristu ucite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.
16 Mau a Knstu akhalitse mwa inu cicurukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalmo, ndimayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuyimbira Mulungu ndi cisomo mumtima mwanu.
17 Ndipo ciri conse mukacicita m'mau kapena muncbito, citani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa iye.
18 Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.
19 Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo.