4 Pamene Kristu adzaoneka, ndiye moyo wathu, pamenepo inunso mudzaonekera pamodzi ndi iye m'ulemerero.
5 Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;
6 cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;
7 zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,
8 Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:
9 musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,
10 ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;