6 cifukwa ca izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;
7 zimene munayendamo inunso kale, pamene munakhala ndi moyo wanu m'menemo,
8 Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zoturuka m'kamwa mwanu:
9 musamanamizana wina ndi mnzace; popeza mudabvula munthu wakale pamodzi ndi nchito zace,
10 ndipo munabvala watsopano, amene alikukonzekawatsopano, kuti akhale naco cizindikiritso, mousa mwa cifaniziro ca iye amene anamlenga iye;
11 pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.
12 Cifukwa cace bvalani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wacifundo, kukoma mtima, kudzicepetsa, cifatso, kuleza mtima;