11 Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse,
12 ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;
13 akulindira ciyembekezo eodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkuru ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu;
14 amene anadzipereka yekha m'malo mwa ife, kuti akatiombole Ife ku zoipa zonse, nakadziyeretsere yekha anthu akhale ace eni eni, acangu pa nchito zokoma.
15 Izi lankhula, ndipo ucenjeze, nudzudzule ndi ulamuliro wonse. Munthu asakupeputse.