7 m'zonse udzionetsere wekha citsanzo ca nchito zabwino; m'ciphunzitse cako uonetsere cosabvunda, ulemekezeko,
8 mau olama osatsutsika; kuti iye wakutsutsana acite manyazi, posakhala nako kanthu koipa kakutinenera ife.
9 Akapolo amvere ambuye ao a iwo okha, nawakondweretse m'zonse; osakana mau ao;
10 osatapa pa zao, komatu aonetsere cikhulupiriko conse cabwino; kuti akakometsere ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu Mulungu m'zinthu zonse.
11 Pakuti caonekera cisomo ca Mulungu cakupulumutsa anthu onse,
12 ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana cisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;
13 akulindira ciyembekezo eodala, ndi maonekedwe a ulemerero wa Mulungu wamkuru ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu;