1 Uwakumbutse iwo agonje kwa akulu, ndi aulamuliro, akhale omvera, okonzeka pa nchito iri yonse yabwino;
2 asacitire mwano munthu ali yense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere cifatso conse pa anthu onse.
3 Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akucitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundu mitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzace.
4 Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka,
5 zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,