2 asacitire mwano munthu ali yense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere cifatso conse pa anthu onse.
3 Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akucitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundu mitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzace.
4 Koma pamene kukoma mtima, ndi cikondi ca pa anthu, ca Mpulumutsi wathu Mulungu zidaoneka,
5 zosati zocokera m'nchito za m'cilungamo, zimene tidazicita ife, komatu monga mwa cifundo cace anatipulumutsa ife, mwa kutsuka kwa kubadwanso ndi makonzedwe a Mzimu Woyera,
6 amene anatsanulira pa ife mocurukira, mwa Yesu Kristu Mpulumutsi wathu;
7 kuti poyesedwa olungama ndi cisomo ca Iyetu, tikayesedwe olowa nyumba monga mwa ciyembekezo ca moyo wosatha.
8 Okhulupirika mauwa, ndipo za izi ndifuna kuti ulimbitse mau, kuti iwo akukhulupirira Mulungu asamalire akhalebe atsogoleri a nchito zabwino. Izi nzokoma ndi zopindulitsa anthu;