1 YUDA, kapolo wa Yesu Kristu, ndi mbale wa Yakobo, kwa iwo oitanidwa, okondedwa mwa Mulungu Atate, ndi osungidwa ndi Yesu Kristu:
2 Cifundo ndi mtendere ndi cikondi zikucurukireni.
3 Okondedwa, pakucira cangu conse cakukulemberani za cipulumutso ca ife tonse, ndafulumidwa mtima ine kukulemberani ndi kudandaulira kuti mulimbanetu cifukwa ca cikhulupiriro capatsidwa kamodzi kwa oyera mtima.
4 Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira citsutso ici, anthu osapembedza, akusandutsa cisomo ca Mulungu wathu cikhale cilak olako conyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Kristu.
5 Koma ndifuna kukukumbutsani mungakhale munadziwa zonse kale kuti Ambuye, atapulumutsa mtundu wa anthu ndi kuwaturutsa m'dziko La Aigupto, anaononganso iwo osakhulunirira.
6 Angelonso amene sanasunga cikhalidwe cao coyamba, komatu anasiya pokhala pao pao, adawasunga m'ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira ciweruziro ca tsiku lalikuru.
7 Monga; Sodoma ndi Gomora, ndi midzi yakuizungulira, potsatana nayoyo, idadzipereka kudama, ndi kursara zilakolako zacilendo, iikidwa citsanzo, pakucitidwa cilango ca mota wosatha.
8 Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nacitira mwano maulemerero.
9 Koma Mikayeli mkulu wa angelo, pakucita makani ndi mdierekezi anatsutsana za thupi la Mose, sanalimbika mtima kumehulira cifukwa comcitira mwano, koma anati, Ambuye akudzudzule.
10 Koma iwowa zimene sazidziwa azicitira mwano; ndipo zimene azizindikira cibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika,
11 Tsoka kwa iwo! pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'cisokero ca Balamu cifukwa ca kulipira, natayika m'citsutsano ca Kore,
12 Iwo ndiwo okhala mawanga pa mapwando anu a cikondano, pakudya nanu pamodzi, akudziweta okha opanda mantha; mitambo yopanda madzi, yotengekatengeka ndi mphepo; mitengo ya masika yopanda zipatso, yofafa kawid, yozuka mizu;
13 mafunde oopsya a nyanja, akuwinduka thobvu la manyazi a iwo okha; nyenyezi zosokera, zimene mdima wakuda bii udazisungikira kosatha.
14 Ndipo kwa iwo, Henoke, wacisanu ndi ciwiri kuyambira kwa Adamu, ananenera kuti, Taona, wadza Ambuye ndi oyera ace zikwi makumi,
15 kudzacitira onse ciweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa nchito zao zonse zosapembedza, zimene anazicita kosapembedza, ndi pa zolimba zimene ocimwa osapembedza adalankhula pa iye.
16 Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuruzikuru), akutama anthu cifukwa ca kupindula nako.
17 Koma inu, abale, mukumbukile mau onenedwa kale ndi atumwi a Ambuye wathu Yesu Kristu;
18 kuti ananena nanu, 1 Pa nthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo okha.
19 Iwo ndiwo opatukitsa, anthu a makhalidwe acibadwidwe, osakhala naye Mzimu.
20 Koma inu, okondedwa, 3 podzimangirira nokha pa cikhulupiriro canu coyeretsetsa, ndi 4 kupemphera mu Mzimu Woyera,
21 mudzisunge nokha m'cikondi ca Mulungu, ndi 5 kulindira cifundo ca Ambuye wathu Yesu Kristu, kufikira moyo wosatha.
22 Ndipo ena osinkhasinkha muwacitire cifundo,
23 koma ena 6 muwapulumutse ndi kuwakwatula kumoto; koma ena muwacitire cifundo ndi mantha, 7 nimudane naonso maraya ocitidwa mawanga ndi thupi
24 Ndipo 8 kwa iye amene akhoza kukudikirani mungakhumudwe, ndi 9 kukuimikani pamaso pa ulemerero wace opanda cirema m'kukondwera,
25 10 kwa Mulungu wayekha, Mpulumutsi wathu, mwa Yesu Kristu Ambuye wathu, zikhale ulemerero, ukulu, mphamvu, ndi ulamuliro zisanayambe nthawi, ndi tsopano, ndi kufikira nthawi zonse. Amen.