Cibvumbulutso 1 BL92

Coneneratu bukuli

1 CIBVUMBULUTSO ca Yesu Kristu, cimene Mulungu anambvumbulutsira acionetsere akapolo ace, ndico ca izi ziyenera kucitika posacedwa: ndipo potuma mwa mngelo wace anazindikiritsa izi kwa kapolo wace Yohane;

2 amene anacita umboni za mau a Mulungu, ndi za umboni wa Yesu Kristu, zonse zimene adaziona.

3 Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a cineneroco, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.

Mau a kwa Mipingo isanu ndi iwiri ya m'Asiya

4 Yohane kwa Mipingo isanu ndi wiri m'Asiya: Cisomo kwa inu ndi ntendere, zocokerakwa iye amene ili, ndi amene adali, ndi amene aliikudza; ndi kwa mizimu isanu ndi wiri yokhala ku mpando wacifumu vace;

5 ndi kwa Yesu Kristu, mboli yokhulupirikayo, wobadwa woyanba wa akufa, ndi mkulu wa mafunu a dziko lapansi, Kwa iye ameieatikonda ife, natimasula ku macimo athu ndi mwazi wace;

6 natiyesa ife ufumu tikhale ansembe a Mulungu ndiye Atate wace; kwa iye kukhale ulemerero ndi mphamvu kufikira nthawi za nthawi. Amen.

7 Taonani, adza ndi mitambo; ndipo diso liri lonse lidzampenya iye, iwonso amene anampyoza; ndipo mafuko onse a pa dziko adzamlira iye. Terotu. Amen.

8 Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.

Yohane pa cisumbu ca Patmo, Amlembetsa masomphenya

9 Ine Yohane, mbale wanu ndi woyanjana nanu m'cisautso ndi ufumu ndi cipiriro zokhala m'Yesu, ndinakhala pa cisumbu cochedwa Patmo, cifukwa ca mao a Mulungu ndi umboni wa Yesu.

10 Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau akuru, ngati a lipenga,

11 ndi kuti, Cimene upenya, lemba m'buku, nulitumize kwa Mipingo isanu ndi iwiri, ku Efeso, ndi ku Smurna, ndi ku Pergamo, ndi ku Tiyatira, ndi ku Sarde, ndi ku Filadelfeya, ndi ku Laodikaya.

12 Ndipo ndinaceuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditaceuka ndinaona zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi;

13 ndipo pakati pa zoikapo nyalizo wina wonga Mwana wa munthu atabvala cobvala cofikira ku mapazi ace, atamangira lamba lagolidi pacifuwa.

14 Ndipo tsitsi la pamutu pace linali loyera ngati ubweya woyera, ngati cipale cofewa; ndi maso ace ngati lawi la moto;

15 ndi mapazi ace ngati mkuwa wonyezimira, ngati woyengeka m'ng'anjo; ndi mau ace ngati mkokomo wa madzi ambiri.

16 Ndipo m'dzanja lace lamanja munali nyenyezi zisanu ndi ziwirl; ndi m'kamwa mwace mudaturuka lupanga lakuthwa konse konse; ndipo nkhope yace ngati dzuwa lowala mu mphamvu yace.

17 Ndipo pamene ndinamuona iye, ndinagwa pa mapazi ace ngati wakufa; ndipo anaika dzanja lace lamanja pa ine, nati, Usaope, ine ndine woyamba ndi wotsiriza,

18 ndi Wamoyoyo; ndipo 1 ndinali wakufa, ndipo taona, ndiri wamoyo kufikira nthawi za nthawi, ndipo ndiri nazo zofungulira za imfa ndi Hade.

19 Cifukwa cace 2 lembera zimene unaziona, ndi zimene ziripo, ndi zimene zidzaoneka m'tsogolomo;

20 3 cinsinsi ca nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona pa dzanja langa lamanja, ndi 4 zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo 5 angelo a Mipingo isanu ndi iwirl; ndipo zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri ndizo 6 Mipingo isanu ndi iwiri.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22