Cibvumbulutso 19 BL92

Kupasuka kwa Babula. Cimwemwe ndi mayamiko m'Mwamba

1 Zitatha izi ndinamva ngati a mau akuru khamu lalikuru m'Mwamba, liri kunena, Aleluya; cipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu, nza Mulungu wathu;

2 pakuti maweruzo ace ali oona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wacigololo wamkuru, amene anaipsa dziko ndi cigololo cace, ndipo anabwezera cilango mwazi wa akapolo ace pa dzanja lace la mkaziyo.

3 Ndipo anatinso, Aleluya. Ndipo utsi wace ukwera ku nthawi za nthawi.

4 Ndipo anagwa pansi akuluwo makumi awiri mphambu anai ndi zamoyo zinai, ndipo zinalambira Mulungu wakukhala pa mpando wacifumu, nizinena, Amen; Aleluya.

5 Ndipo mau anacokera ku mpando wacifumu, ndi kunena, Lemekezani Mulungu wathu akapolo ace onse, akumuopa iye, ang'ono ndi akuru.

6 Ndipo ndinamva ngati mau a khamu lalikuru, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati mau a mabingu olimba, nizinena, Aleluya; pakuti acita ufumu Ambuye Mulungu wathu, Wamphamvuyonse.

7 Tikondwere, tisekerere, ndipo tipatse ulemerero kwa iye; pakuti wadza ukwati wa Mwanawankhosa; ndipo mkazi wace wadzikonzera.

8 Ndipo anampatsa iye abvale bafuta wonyezimira woti mbu; pakuti bafuta ndiye zolungama za oyera mtima.

9 Ndipo ananena ndi ine, Lemba, Odala iwo amene aitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwanawankhosa. Ndipo ananena ndi ine, Iwo ndiwo mau oona a Mulungu.

10 Ndipo ndinagwa pa mapazi ace kumlambira iye. Ndipo ananena ndi ine, Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako, ndi mnzao wa abale ako akukhala nao umboni wa Yesu; lambira Mulungu: pakuti umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa cinenero.

Kristu agonjetsa cirombo ndi mneneri wonyenga

11 Ndipo ndinaona mutatseguka m'Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi iye wakumkwera wochedwa Wokhulupirika ndi Woona; ndipo aweruza, nacita nkhondo molungama.

12 Ndipo maso ace ali lawi la moto, ndi pamutu pace pali nduwira zacifumu zambiri; ndipo ali nalo dzina lolembedwa, wosalidziwa wina yense koma iye yekha.

13 Ndipo abvala cobvala cowazidwa mwazi; ndipo achedwa dzina lace, Mau a Mulungu.

14 Ndipo magulu a nkhondo okhala m'Mwamba anamtsata iye, okwera pa akavalo oyera, obvala bafuta woyera woti mbu.

15 Ndipo m'kamwa mwace muturuka Iupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo iye adzawalamulira ndi ndodo yacitsulo: ndipo aponda iye moponderamo mphesa mwa vinyo waukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.

16 Ndipo ali nalo pa cobvala cace ndi pa ncafu yace dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.

17 Ndipo ndinaona mngelo alikuima m'dzuwa; ndipo anapfuula ndi mau akuru alrunena 1 ndi mbalame zonse zakuuluka pakati pa mlengalenga: 2 Idzani kuno, sonkhanani ku phwando la Mulungu wamkuru,

18 kuti 3 mudzadye nyama ya mafumu, ndi nyama ya akapitao, ndi nyama ya anthu amphamvu, ndi nyama ya akavalo, ndi ya iwo akukwerapo, ndi nyama ya anthu onse, mfulu ndi akapolo, ndi ang'ono ndi akuru.

19 Ndipo 4 ndinaona ciromboco, ndi mafumu a dziko, ndi magulu a nkhondo ao, osonkhanidwa kucita nkhondo pa iye wakukwera pa kavalo, ndi gulu la nkhondo lace.

20 Ndipo 5 cinagwidwa ciromboco, ndi pamodzi naco mneneri wonyenga amene adacita zizindikilo pamaso pace, zimene anasokeretsa nazo iwo amene adalandira lemba la cirombo, ndi iwo akulambira fano lace; 6 iwo awiri anaponyedwa ali moyo m'nyanja yamoto yakutentha ndi sulfure:

21 ndipo otsalawa anaphedwa ndi lupanga la iye wakukwera pa kavalo, ndilo lo turuka m'kamwa mwace; ndipo mbalame zonse zinakhuta ndi nyama zao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22