Cibvumbulutso 6 BL92

Atsegula zosindikiza zisanu ndi cimodzi

1 Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula cimodzi ca zizindikilo zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva cimodzi mwa zamoyo zinai, nicinena, ngati mau a bingu, Idza.

2 Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anaturukira wolakika kuti alakike.

3 Ndipo pamene anamasula cizindikilo caciwiri, ndinamva camoyo caciwiri nicinena, Idza.

4 Ndipo anaturuka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakucotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikuru.

5 Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacitatu, ndinamva camoyo cacitatu nicinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lace.

6 Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.

7 Ndipo pamene anamasula cizindikilo cacinai, ndinamva mau a camoyo cacinai nicinena, Idza.

8 Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lace ndiye Imfa; ndipo Hade anatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lacinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zirombo za padziko.

9 Ndipo pamene adamasula cizindikilo cacisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa cifukwa ca mau a Mulungu, ndi cifukwa ca umboni umene anali nao:

10 ndipo anapfuula ndi mau akulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera cilango cifukwa ca mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?

11 Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.

12 Ndipo ndinaona pamene anamasula cizindikilo cacisanu ndi cimodzi, ndipo panali cibvomezi cacikuru; ndi dzuwa lidada bii longa ciguduli ca ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;

13 ndi nyenyezi zam'mwamba zinagwa padziko, monga mkuyu utaya nkhuyu zace zosapsya, pogwedezeka ndi mphepo yolimba.

14 Ndipo kumwamba kudacoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kucoka m'malo mwao.

15 Ndipo mafumu a dziko, ndi akuru, ndi akazembe, ndi acuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;

16 nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya iye amene akhala pa mpando wacifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa;

17 cifukwa lafika tsiku lalikuru la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani?

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22