1 Ndipo ndinamva mau akuru ocokera kuKacisi, akunena kwa angelo asanu ndi awiri, Mukani, ndipo tsanulirani kudziko mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu.
2 Ndipo anacoka woyamba, natsanulira mbale yace kudziko; ndipo kunakhala cironda coipa ndi cosautsa pa anthu akukhala nalo lemba la cirombo nalambira fano lace.
3 Ndipo waciwiri anatsanulira mbale yace m'nyanja; ndipo kunakhala mwazi ngati wa munthu wakufa; ndipo zamoyo zonse za m'nyanja zidafa.
4 Ndipo wacitatu anatsanulira mbale yace ku mitsinje ndi akasupe a madzi; ndipo kunasanduka mwazi.
5 Ndipo ndinamva mngelo wa madziwo nanena, Muli wolungama, amene muli, nimunali, Woyera Inu, cifukwa mudaweruza kotero;
6 popeza anatsanulira mwazi wa oyera mtima, ndi wa aneneri, ndipo mudawapatsa mwazi amwe; ayenera iwo.
7 Ndipo ndinamva wa pa guwa la nsembe, alinkunena, Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.
8 Ndipo wacinai anatsanulira mbale yace padzuwa; ndipo analipatsa ilo litenthe anthu ndi moto.
9 Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukuru; ndipo anacitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalapa kuti amcitire ulemu.
10 Ndipo wacisanu anatsanulira mbale yace pa mpando wacifumu wa cirombo; ndipo ufumu wace unadetsedwa; ndipo anatafuna malilime ao ndi kuwawa kwace,
11 nacitira mwano Mulungu wa m'Mwamba cifukwa ca zowawa zao ndi zironda zao; ndipo sanalapa nchito zao.
12 Ndipo wacisanu ndi cimodzi anatsanulira mbale yace pa mtsinje waukuru Firate; ndi madzi ace anaphwa, kuti ikonzeke njira ya mafumu ocokera poturuka dzuwa.
13 Ndipo ndinaona moturuka m'kamwa mwa cinjoka, ndi m'kamwa mwa cirombo, ndi m'kamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati acule;
14 pakuti ali mizimu ya ziwanda zakucita zizindikilo; zimene zituruka kumka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira ku nkhondo ya tsiku lalikuru la Mulungu, Wamphamvuyonse.
15 (Taonani, ndidza ngati mbala. Wodala iye amene adikira, nasunga zobvala zace, kuti angayende wausiwa, nangapenye anthu usiwa wace.)
16 Ndipo anawasonkhanitsira ku malo ochedwa m'Cihebri Harmagedo.
17 Ndipo wacisanu ndi ciwiri anatsanulira mbale yace mumlengalenga; ndipo m'Kacisimo mudaturuka mau akuru, ocokera ku mpando wacifumu ndi kunena, Cacitika;
18 ndipo panakhala mphezi, ndi mau, ndi mabingu; ndipo panali 1 cibvomezi cacikuru cotero sicinaoneke ciyambire anthu padziko, cibvomezi colimba cotero, cacikuru cotero.
19 Ndipo 2 cimudzi cacikuruco cidagawika patatu, ndi midzi ya amitundu inagwa; ndipo 3 Babulo waukuru unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse cikho ca vinyo wamkali wa mkwiyo wace.
20 Ndipo 4 zisumbu zonse zidathawa, ndi mapiri sanapezeka.
21 Ndipo 5 anatsika kumwamba matalala akuru, lonse lolemera ngati talenti, nagwa pa anthu; ndipo anthu 6 anacitira Mulungu mwano cifukwa ca mliri wa matalala, pakuti m1iri wace nm waukuru ndithu.