Cibvumbulutso 2 BL92

Kalata wa kwa Mpingo wa ku Efeso

1 Kwa mngelo wa Mpingo wa ku Efeso lemba;Izi azinena iye amene agwira nyenyezi zisanu ndi ziwiri m'dzanja lace lamanja, iye amene ayenda pakati pa zoikapo nyali zisanu ndi ziwiri zagolidi:

2 Ndidziwa nchito zako, ndi cilemetso cako ndi cipiriro cako, ndi kuti sukhoza kulola oipa, ndipo unayesa iwo amene adzicha okha atumwi, osakhala atumwi, nuwapeza onama;

3 ndipo uli naco cipiriro, ndipo walola cifukwa ca dzina langa, wosalema.

4 Koma ndiri nako kanthu kotsutsana ndi iwe, kuti unataya cikondi cako coyamba.

5 Potero kumbukila kumene wagwerako, nulape, nucite nchito zoyamba; koma ngari sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa coikapo nyali cako, kucicotsa pamalo pace, ngati sulapa.

6 Koma ici uli naco, kuti udana nazo nchito za Anikalai, zimene Inenso ndidana nazo.

7 Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo, K wa iye amene alakika ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli m'Paradaiso wa Mulungu.

Kalata waciwiri, wa kwa Mpingo wa ku Smurna

8 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Smurna lemba;Izi anena woyamba ndi wotsiriza, amene anakhala wakufa, nakhalanso ndi moyo:

9 Ndidziwa cisautso cako, ndi umphawi wako (komatu uli wacuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.

10 Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena ainu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala naco cisautso masiku khumi. Khala wokholupirfka kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.

11 Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene alakika sadzacitidwa coipa ndi imfa yaciwiri.

Kalata wacitatu, wa kwa Mpingo wa ku Pergamo

12 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Pergamo lemba:Izi anena iye wokhala nalo lupanga lakuthwa konse konse:

13 Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wacifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza cikhulupiriro canga, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.

14 Komatu ndiri nazo zinthu pang'ono zotsutsana ndi iwe, popeza uli nao komweko akugwira ciphunzitso ca Balamu, amene anaphunzitsa Balaki aponye cokhumudwitsa pamaso pa ana a Israyeli, kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano, nacite cigololo.

15 Kotero uli nao akugwira ciphunzitso ca Anikolai momwemonso.

16 Cifukwa cace lapa; ukapanda kutero ndidza kwa iwe posacedwa, ndipo ndidzacita nao nkhondo ndi lupanga la m'kamwa mwanga.

17 Iye wakukhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wolakika, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pa mwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu ali yense koma iye wakuulandira.

Kalata wacinai, wa kwa Mpingo wa ku Tiyatira

18 Ndipo kwa mngelo wa Mpingo wa ku Tiyatira lemba:Izi azinena Mwana wa Mulungu, wakukhala nao maso ace ngati lawi la moto, ndi mapazi ace ngati mkuwa wonyezimira:

19 1 Ndidziwa nchito zako, ndi cikondi, ndi cikhulupiriro, ndi utumiki, ndi cipiriro cako, ndi kuti nchito zako zotsiriza cicuruka koposa zoyambazo.

20 Komatu ndiri nako kotsutsana ndi iwe, cuti ulola mkazi 2 Yezebeli, wodzieha zekha mneneri; ndipo aphunzitsa, nasokeretsa akapolo anga, kuti acite cigololo ndi kudya zoperekedwa nsenbe kwa mafano.

21 Ndipo ndanpatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana naco cigololo cace.

22 Taona, ndimponya iye pakama, ndi iwo akucita cigololo naye kuwalonga m'cisautso cacikuru, ngati salapa iwo ndi kuleka nchito zace.

23 Ndipo ndidzaononga ana ace ndi imfa; ndipo idzazindikira Mipingo yonse kuti 3 ine ndine iye amene ayesa imso ndi mitima; ndipo 4 ndidzaninkha kwa yense wa inu monga mwa nchito zanu.

24 Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiyatira, onse amene alibe ciphunzitso ici, amene sanazindikira zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.

25 Koma 5 cimene muli naco, gwirani kufikira ndikadza.

26 Ndipo iye amene alakika, ndi iye amene asunga nchito zanga kufikira citsiriziro, kwa iye 6 ndidzapatsa ulamuliro wa pa amitundu;

27 ndipo 7 adzawalamulira ndi ndodo yacitsulo, monga zotengera za woumba mbiya ziphwanyika mapale; monga lnenso ndalandira kwa Atate wanga;

28 ndipo ndidzampatsa iye 8 nthanda.

29 Iye wokhala nalo khutu amve cimene Mzimu anena kwa Mipingo.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22