Cibvumbulutso 7 BL92

Aisrayeli okhulupirika alanditsidwa

1 Zitatha izi ndinao na angelo anai alinkuimirira pa ngondya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uli wonse.

2 Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kucokera poturuka dzuwa, ali naco cizindikilo ca Mulungu wamoyo: ndipo anapfuula ndi mau akuru kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,

3 nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza cizindikilo akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pao.

4 Ndipo ndinamva ciwerengo ca iwo osindikizidwa cizindikilo, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa cizindikilo mwa mafuko onse a ana a Israyeli,

5 Mwa pfuko la Yuda anasindikizidwa cizindikilo zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri:

6 Mwa pfuko la Aseri zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Nafitali zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri:

7 Mwa pfuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Levi zikwi khumi ndiziwiri:Mwa pfuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri:

8 Mwa pfuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri:Mwa pfuko la Benjamini anasindikizidwa cizindikilo zikwi khumi ndi ziwiri.

Maonekedwe mulemerero a iwo amene anaphedwa cifukwa ca Kristu

9 Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikuru, loti palibe munthu anakhozakuliwerenga, ocokera mwa mtundu uti wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wacifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atabvala zobvalazoyera, ndi makhwatha a kanjedza m'manja mwao;

10 ndipo apfuula ndi mau akuru, nanena, Cipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.

11 Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wacifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi ku mpando wacifumu, nalambifa Mulungu,

12 ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi ciyamiko, ndi ulemu, ndi cilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.

13 Ndipo mmodzi wa akuru anayankha, nanena ndi ine, Iwo obvala zobvala zoyera ndiwo ayani, ndipo acokera kuti?

14 Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwaine, Iwo ndiwo akuturuka m'cisautso cacikuru; ndipo anatsuka zobvala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.

15 Cifukwa cace ali ku mpando wacifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira iye usana ndi usiku m'Kacisi mwace; ndipo iye wakukhala pa mpando wacifumu adzawacitira mthunzi,

16 sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena, silidzawatentha dzuwa, kapena citungu ciri conse;

17 cifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wacifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22