Cibvumbulutso 18 BL92

Kupasuka kwa Babulo. Maliro pa dziko lapansi

1 Zitatha izi ndinaona mngelo wina wakutsika m'Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukuru; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wace.

2 Ndipo anapfuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babulo waukuru, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.

3 Cifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa cigololo cace mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anacita naye cigololo; ndipo ocita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyererakwace.

4 Ndipo ndinamva mau ena ocokera Kumwamba, nanena, Turukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi macimo ace, ndi kuti mungalandireko ya miliri yace;

5 pakuti macimo ace anaunjikizana kufikira m'Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zace.

6 Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa nchito zace; m'cikhomo unathiramo, muuthirire cowirikiza.

7 Monga momwe unadzicitira ulemu, nudyerera, momwemo muucitire eouzunza ndi couliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwace, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.

8 Cifukwa cace miliri yace idzadzam'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; cifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.

9 Ndipo mafumu a dziko ocita cigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwace, poima patali,

10 cifukwa cakuopa cizunzo cace, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, Babulo, mudzi wolimba! pakuti m'ora limodzi cafika ciweruziro canu.

11 Ndipo ocita malonda a m'dziko adzalira nadzaucitira cifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;

12 malonda a golidi, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wace, ndi a ngale, ndi a nsaru yabafuta, ndi a cibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya pfungo lokoma, ndi cotengera ciri conse ca minyanga ya njobvu, ndi cotengera ciri conse camtengo wa mtengo wace wapatali, ndi camkuwa ndi cacitsulo, ndi cansangalabwi;

13 ndi kinamomo ndi amomo, ndi zofukiza, ndi zodzola, ndi libano, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magareta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.

14 Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakucokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.

15 Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali cifukwa ca kuopa cizunzo cace, nadzalira, ndi kucita cifundo;

16 nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuru wobvala bafuta ndi cibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golidi, ndi mwala wa mtengo wace, ndi ngale!

17 Pakuti m'ora limodzi casanduka bwinja cuma cacikuru cotere. Ndipo watsigiro ali yense, ndi yense wakupita panyanja pakuti pakuti, ndi amarinyero, ndi onse amene amacita kunyanja, anaima patali,

18 napfuula poona utsi wa kutentha kwace, nanena, Mudzi uti ufanana ndi mudzi waukuruwo?

19 Ndipo anathira pfumbi pamitu pao, napfuula, ndi kulira, ndi kucita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuruwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, cifukwa ca kulemera kwace, pakuti m'ora limodzi unasanduka bwinja.

20 Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; cifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.

21 Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikuru, naiponya m'nyanja, nanena, Cotero Babulo, mudzi waukuru, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.

22 Ndipo mau a anthu oyimba zeze, ndi a oyimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo nunisiri ali yense wa macitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe;

23 1 ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti 2 ndi nyanga yako mitunduyonse inasokeretsedwa.

24 Ndipo 3 momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.

Mitu

1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22